Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 26:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Kwaloleka udzinenere wekha. Pamenepo Paulo, anatambasula dzanja nadzikanira:

2. Ndidziyesera wamwai, Mfumu Agripa, popeza nditi ndidzikanira lero pamaso panu, za zonse zimene Ayuda andinenera nazo;

3. makamaka popeza mudziwitsa miyambo yonse ndi mafunso onse a mwa Ayuda; cifukwa cace ndikupemphani mundimvere ine moleza mtima.

4. Mayendedwe a moyo wanga tsono, kuyambira pa cibwana canga, amene anakhala ciyambire mwa mtundu wanga m'Yerusalemu, awadziwa Ayuda onse;

5. andidziwa ine ciyambire, ngati afuna kucitapo umboni, kuti ndinakhala Mfarisi monga mwa mpatuko wolunjikitsitsa wa cipembedzero cathu.

6. Ndipo tsopano ndiimirira pano ndiweruzidwe pa ciyembekezo ca lonjezano limene Mulungu analicita kwa makolo athu;

7. kunkira komweko mafuko athu khumi ndi awiri, potumikira Mulungu kosapumula usiku ndi usana, ayembekeza kufikirako. Cifukwa ca ciyembekezo ici, Mfumu, andinenera Ayuda.

8. Muciyesa cinthu cosakhulupirika, cakuti Mulungu aukitsa akufa?

9. Inedi ndinayesa ndekha, kuti kundiyenera kucita zinthu zambiri zotsutsana nalo dzina la Yesu Mnazarayo.

10. Cimenenso ndinacita m'Yerusalemu: ndipo ndinatsekera ine oyera mtima ambiri m'ndende, popeza ndidalandira ulamuliro wa kwa ansembe akulu; ndiponso pophedwa iwo, ndinabvomerezapo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 26