Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 25:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Cifukwa cace, ati, iwo amene akhoza mwa inu amuke nane potsikirako, ndipo ngati kuli kanthu kosayenera mwa munthuyo amnenere iye.

6. Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikiraku Kaisareya; ndipo m'mawa mwace anakhala pa mpando waciweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.

7. Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikuru, zimene sanakhoza kuzitsimikiza;

8. koma Paulo podzikanira ananena, Sindinacimwa kanthu kapena pacilamulo, kapena paKacisi, kapena pa Kaisara.

9. Kama Festo pofuna kuyesedwa wacisomo ndi Ayuda, anayankha kwa Paulo, nati, Kodi ufuna kukwera kunka ku Yerusalemu, ndi kuweruzidwa ndi ine pomwepo kunena za zinthu izi?

10. Koma Paulo anati, ndirikuimirira pa mpando waciweruziro wa Kaisara, pompano ndiyenera kuweruzidwa ine; Ayuda sindinawacitira-kanthu koipa, monga mudziwanso nokha bwino.

11. Pamenepo ngati ndiri wocita zoipa, ngati ndacita kanthu kakuyenera imfa, sindikana kufa; koma ngati zinthuzi awa andinenera nazo ziri zacabe, palibe mmodzi akhoza kundipereka kwa iwo. Nditurukira kwa Kaisara.

12. Pamenepo Festo, atakamba ndi aphungu ace, anayankha, Wanena, Ndirurukira kwa Kaisara; kwa Kaisara udzapita.

13. Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Bemike anafika ku Kaisareya, nalankhula Festo.

14. Ndipo atatsotsako masiku ambiri, Festo anafotokozera mfumuyo mlandu wace wa Paulo, nanena, Pali munthu adamsiya m'ndende Felike,

15. amene ansembe akulu ndi akulu a Ayuda anamnenera kwa ine, ndiri ku Yerusalemu, nandipempha ndiipitse mlandu wace.

16. Koma ndinawayankha, kuti macitidwe a Aroma satero, kupereka munthu asanayambe woneneredwayo kupenyana nao omnenera ndi kukhala napo podzikanira pa comneneraco.

17. Potero, pamene adasonkhana pano, sindinacedwa, koma m'mawa mwace ndinakhala pa mpando waciweruziro, ndipo ndinalamulira adze naye munthuyo.

18. Ndipo pamene anaimirira omneneza, sanamchulira konse cifukwa ca zoipa zonga ndinazilingirira ine;

19. koma anali nao mafunso ena otsutsana naye a cipembedzero ca iwo okha, ndi mafunso a wina Yesu, amene adafa, amene Paulo anati kuti ali ndi moyo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 25