Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikiraku Kaisareya; ndipo m'mawa mwace anakhala pa mpando waciweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.