Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 24:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Ndipo pamene adamuitana, Tertulo anayamba kumnenera ndi kunena.Popeza tiri nao mtendere wambiri mwa inu, ndipo mwa kuganiziratu kwanu muukonzera mtundu wathu zotiipsa,

3. tizilandira ndi ciyamiko conse, monsemo ndi ponsepo, Felike womveka inu.

4. Koma kuti ndingaonjeze kukulemetsani ndikupempha, ni mutimvere mwacidule ndi cifatso canu.

5. Pakuti tapeza munthuyu ali ngati mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m'dziko lonse lokhalamo anthu, ndi mtsogoleri wa mpanduko wa Anazarene;

6. amenenso anayesa kuipsa Kacisi; amene tamgwira;

8. kwa iye mudzakhoza kuzindikira pomfunsa nokha, za izi zonse timnenerazi.

9. Ndipo Ayudanso anabvomerezana naye, natsimikiza kuti izi zitero.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 24