Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 24:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Ndipo zitapita zaka zambiri ndinadza kutengera mtundu wanga zacifundo, ndi zopereka;

18. popereka izi anandipeza woyeretsedwa m'Kacisi, wopanda khamu la anthu, kapena phokoso; koma panali Ayuda ena a ku Asiya,

19. ndiwo mwenzi atakhala pano pamaso panu ndi kundinenera, ngati ali nako kanthu kotsutsa ine.

20. Kapena iwo amene ali kunowa anene anapeza cosalungama cotani, poimirira ine pamaso pa bwalo la akuru,

21. koma mau awa amodzi okha, amene ndinapfuula poimirira pakati pao, Kunena za kuuka kwa akufa ndiweruzidwa ndi inu lero lino.

22. Koma Felike anawalinditsa, popeza anadziwitsadi Njirayo, nati, Pamene Lusiya kapitao wamkuru akatsika ndidzazindikiritsa konse za kwa inu.

23. Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ace kumtumikira.

24. Koma atapita masiku ena, anadza Felike ndi Drusila mkazi wace, ndiye Myuda, naitana Paulo, ndipo anamva iye za cikhulupiriro ca Kristu Yesu.

25. Ndipo m'mene anamfotokozera za cilungamo, ndi cidziletso, ndi ciweruziro cirinkudza, Felike anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.

26. Anayembekezanso kuti Paulo adzampatsa ndalama; cifukwa cacenso anamuitana iye kawiri kawiri, nakamba naye.

27. Koma zitapita zaka ziwiri Porkiyo Festo analowa m'malo a Felike; ndipo Felike pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 24