Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 22:20-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kubvomerezana nao, ndi kusunga Zoobvala za iwo amene anamupha iye.

21. Ndipo anati kwa ine, Pita; cifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.

22. Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Acoke pa dziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

23. Ndipo pakupfuula iwo, ndi kutaya zobvala zao, ndi kuwaza pfumbi mumlengalenga,

24. kapitao wamkuru analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe cifukwa cace nciani kuti ampfuulira comweco.

25. Ndipo m'mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwa kenturiyo wakuimirirako, Kodinkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wace wosamveka?

26. Ndipo pakumva ici kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkuru, namuuza, nanena, Nciani ici uti ucite? pakuti munthuyo ndiye Mroma.

27. Ndipo kapitao wamkuruyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.

28. Ndipo kapitao wamkuru anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wace waukuru. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.

29. Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkurunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

30. Koma m'mawa mwace pofuna kuzindikira cifukwa cace ceni ceni cakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe akulu, ndi bwalo lonse la akulu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 22