Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 20:20-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba m'nyumba,

21. ndi kucitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

22. Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidza'ndigwera ine kumeneko;

23. koma kuti Mzimu Woyera andicitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

24. Komatu sindiuyesa kanthu moyo, wanga, kuti uli wa mtengo wace kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kucitira umboni Uthenga Wabwino wa cisomo ca Mulungu.

25. Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.

26. Cifukwa cace ndikucitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.

27. Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.

28. Tadzicenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo Mzimu Woyera anakuikani oyang'anira, kuti muwete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye yekha.

29. Ndidziwa ine kuti, nditacoka ine, adzalowa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo;

30. ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.

31. Cifukwa cace dikirani, nimukumbukile kuti zaka zitatu sindinaleka usiku ndi usana kucenjeza yense wa inu ndi misozi.

32. Ndipo tsopano ndikuikizani kwa Mulungu, ndi kwa mau a cisomo cace, cimene ciri ndi mphamvu yakumangirira ndi kupatsa inu colowa mwa onse oyeretsedwa.

33. Sindinasirira siliva, kapena golidi, kapena cobvala ca munthu ali yense.

34. Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine.

35. M'zinthu zonse ndinakupatsani citsanzo, cakuti pogwiritsa nchito, koteromuyenerakuthandiza ofoka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

36. Ndipo m'mene ananena izi, anagwada pansi, napemphera ndi iwo onse.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 20