Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 20:20-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. kuti sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m'nyumba m'nyumba,

21. ndi kucitira umboni Ayuda ndi Ahelene wa kutembenuza mtima kulinga kwa Mulungu, ndi cikhulupiriro colinga kwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

22. Ndipo, taonani, ndipita ku Yerusalemu womangidwa mumzimu, wosadziwa zimene zidza'ndigwera ine kumeneko;

23. koma kuti Mzimu Woyera andicitira umboni m'midzi yonse, ndi kunena kuti nsinga ndi zisautso zindilindira.

24. Komatu sindiuyesa kanthu moyo, wanga, kuti uli wa mtengo wace kwa ine ndekha; kotero kuti ndikatsirize njira yanga, ndi utumiki ndinaulandira kwa Ambuye Yesu, kucitira umboni Uthenga Wabwino wa cisomo ca Mulungu.

25. Ndipo tsopano, taonani, ndidziwa ine kuti inu nonse amene ndinapitapita mwa inu kulalikira ufumuwo, simudzaonanso nkhope yanga.

26. Cifukwa cace ndikucitirani umboni lero lomwe, kuti ndiribe kanthu ndi mwazi wa anthu onse.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 20