Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 20:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo litaleka phokoso, Paulo anaitana ophunzirawo, ndipo m'mene anawacenjeza, analawirana nao, naturuka kunka ku Makedoniya.

2. Ndipo m'mene atapitapita m'mbali zijazo, nawacenjeza, anadza ku Helene.

3. Ndipo m'mene adakhalako miyezi itatu, ndipo a atampangira ciwembu Ayuda, pori iye apite ndi ngalawa ku Suriya, anatsimikiza mtima abwerere popyola Makedoniya.

4. Ndipo anamperekeza kufikira ku Asiya Sopatro mwana wa Puro, wa ku Bereya; ndipo Atesalonika, Aristarko ndi Sekundo; ndi Gayo wa ku Derbe, ndi Timoteo; ndi a ku Asiya, Tukiko ndi Trofimo.

5. Koma iwowa adatitsogolera, natilinda ku Trowa.

6. Ndipo tinapita m'ngalawa kucokera ku Filipi, atapita masiku a mkate wopanda cotupitsa, ndipo popita masiku asanu tinawapeza ku Trowa; pamenepo tinatsotsa masiku asanu ndi awiri.

7. Ndipo tsiku loyamba la sabata, posonkhana ife kunyema mkate, Paulo anawafotokozera mau, popeza anati acoke m'mawa mwace; ndipo ananena cinenere kufikira pakati pa usiku.

8. Ndipo munali nyali zambiri m'cipinda ca pamwamba m'mene tinasonkhanamo.

9. Ndipo mnyamata dzina lace Utiko anakhala pazenera, wogwidwa nato tulo tatikuru; ndipo pakukhala cifotokozere Paulo, ndipo pogwidwa nato tulo, anagwa posanja paciwiri, ndipo anamtola wakufa.

10. Ndipo potsikirako Paulo, anamgwera namfungatira, nati, Musacite phokoso, pakuti moyo wace ulipo.

11. Ndipo m'mene adakwera, nanyema mkate, nadya, nakamba nao nthawi, kufikira kuca, anacokapo,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 20