Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 19:10-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo anacita comweco zaka ziwiri; kotero kuti onseakukhala m'Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Ahelene.

11. Ndipo Mulungu anacita zamphamvu za pa zokha ndi manja a Paulo;

12. kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsaru zopukutira ndi za panchito, zocokera pathupi pace, ndipo nthenda zinawacokera, ndi mizimu yoipa inaturuka.

13. Koma Ayuda enanso oyendayenda, oturutsa ziwanda, anadziyesa kuchula pa iwo amene anali ndi mizimu yoipa dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.

14. Ndipo panali ana amuna asanu ndi awiri a Skeva, Myuda, mkuru wa ansembe amene anacita ici.

15. Ndipo unayankha mzimu woipa, nuti kwa iwo, Yesu ndimzindikira, ndi Paulo ndimdziwa, koma inu ndinu ayani?

16. Ndipo munthu, mwa iye amene munali mzimu woipa, anawalumphira nawaposa, nawalaka onse awiriwo, kotero kuti anathawa m'nyumba amarisece ndi olasidwa.

17. Zimenezo zidamveka kwa onse, Ayuda ndi Ahelene, amene anakhala ku Efeso; ndipo mantha anagwera onsewo, ndipo dzina la Yesu Iinakuzika.

18. Ndipo ambiri a iwo akukhulipirawo anadza, nabvomereza, nafotokoza macitidwe ao.

19. Ndipo ambiri a iwo akucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao, nawatentha pamaso pa onse; ndipo anawerenga mtengo wace, napeza ndalama zasiliva zikwi makumi asanu.

20. Cotero mau a Ambuye anacuruka mwamphamvu nalakika.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 19