Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 18:22-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo pamene anakoceza pa Kaisareya, anakwera nalankhulana nao Mpingo, natsikira ku Antiokeya.

23. Atakhala kumeneko nthawi, anacoka, napita pa dziko la Galatiya ndi Frugiya m'dziko m'dziko, nakhazikitsaakuphunzira onse.

24. Ndipo anafika ku Efeso Myuda wina dzina lace Apolo, pfuko lace la ku Alesandreya, munthu wolankhula mwanzeru; ndipo anali wamphamvu m'malembo.

25. Iyeyo aoaphunzitsidwa m'njira ya Ambuye; pokhala nao mzimu wacangu, ananena ndi kuphunzitsa mosamalira zinthu za Yesu, ndiye wodziwa ubatizo wa Yohane wokha;

26. ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Priskila ndi Akula, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 18