Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 18:11-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. Ndipo anakhala komwe caka cimodzi kudza miyezi isanu ndi umodzi; naphunzitsamau a Mulungu mwa iwo.

12. Tsono pamene Galiyo anali ciwanga ca Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye ku mpando wa ciweruziro,

13. kuti, Uyu akopa anthu apembedze Mulungu pokana cilamulo.

14. Koma pamene Paulo anati atsegule pakamwa pace, Galiyo anati kwa Ayuda, Ukadakhala mlandu wa cosalungama, kapena dumbo loipa, Ayuda inu, mwenzi nditakumverani inu;

15. koma akakhala mafunso a mau ndi maina ndi cilamulo canu; muyang'ane inu nokha; sindifuna kuweruza zimenezi.

16. Ndipo anawapitikitsa pa mpando wa ciweruziro.

17. Ndipo anamgwira Sostene, mkuru wa sunagoge, nampanda ku mpando wa ciweruziro. Ndipo Galiyo sanasamalira zimenezi.

18. Paulo atakhala cikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nacoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Suriya, pamodzi naye Priskila ndi Akula; popeza anameta mutu wace m'Kenkreya; pakuti adawinda.

19. Ndipo iwo anafika ku Efeso, ndipo iye analekana nao pamenepo: koma iye yekha analowa m'sunagoge, natsutsana ndi Ayuda.

20. Pamene iwo anamfunsa iye kuti akhale nthawi yina yoenjezerapo, sanabvomereza;

21. koma anawatsazika, nati, Akafuna Mulungu, ndidzabwera kwa inu; ndipo anacoka ku Efeso m'ngalawa.

22. Ndipo pamene anakoceza pa Kaisareya, anakwera nalankhulana nao Mpingo, natsikira ku Antiokeya.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 18