Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 17:22-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

22. Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati,Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

23. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipezanso guwa la nsembe lolembedwa potere, KWA MULUNGU WOSADZIWIKA. Cimene mueipembedza osacidziwa, cimeneco ndicilalikira kwa inu.

24. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m'nyumba zakacisi zomangidwa ndi manja;

25. satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse;

26. ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao;

27. kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patari ndi yense wa ife;

28. pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga enanso a akuyimba anu ati, Pakuti ifenso tiri mbadwa zace.

29. Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, woloca ndi luso ndi zolingalira za anthu.

30. Nthawi za kusadziwako tsono Mulungu analekerera; koma tsopanotu alinkulamulira anthu onse ponse ponse atembenuke mtima;

31. cifukwa anapangira tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m'cilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse citsimikizo, pamene anamuukitsa iye kwa akufa.

32. Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za cimeneci.

33. Conco Paulo anaturuka pakati pao.

34. Koma ena anadziphatika kwa iye, nakhulupira; mwa iwonso munali Dionisiyo Mareopagi, ndi mkazi dzina lace Damarisi, ndi ena pamodzi nao.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 17