Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 17:17-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Cotero tsono anatsutsana ndi Ayuda ndi akupembedza m'sunagoge, ndi m'bwalo la malonda masiku onse ndi iwo amene anakomana nao.

18. Ndipo akukonda nzeru ena a Epikureya ndi a Stoiki anatengana naye. Ena anati, ici ciani afuna kunena wobwetuka uyu? Ndipo ena, Anga wolalikira ziwanda zacilendo, cifukwa analalikira Yesu ndi kuuka kwa akufa.

19. Ndipo anamgwira, nanka naye ku Areopagi, nati, Kodi tingathe kudziwa ciphunzitso ici catsopano ucinena iwe?

20. Pakuti ufika nazo ku makutu athu zacilendo: tifuna tsono kudziwa, izi zitani?

21. (Koma Aatene onse ndi alendo akukhalamo anakhalitsa nthawi zao, osacita kanthu kena koma kunena kapena kumva catsopano.)

22. Ndipo anaimirira Paulo pakati pa Areopagi nati,Amuna inu a Atene, m'zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 17