Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 17:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene anapitirira pa Amfipoli, ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda.

2. Ndipo Paulo, monga amacita, analowa kwa iwo; ndipo masabata atatu ananena ndi iwo za m'malembo, natanthauzira,

3. natsimikiza, kuti kunayenera Kristu kumva zowawa, ndi kuuka kwa akufa; ndiponso kuti Yesu yemweyo, amene ndikulalikirani inu, ndiye Kristu.

4. Ndipo ena a iwo anakopedwa, nadziphatika kwa Paulo ndi Sila; ndi Ahelene akupembedza aunyinji ndithu, ndi akazi akuru osati owerengeka.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 17