Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 16:28-36 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Koma Paulo anapfuula ndi mau akuru, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tiri muno.

29. Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m'kati, alinkunthunthunrlra ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Sila,

30. nawaturutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndicitenji kuti ndipulumuke?

31. Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.

32. Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pace.

33. Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pace.

34. Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwace, nawakhazikira cakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pace, atakhulupirira Mulungu.

35. Kutaca, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.

36. Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu turukani, mukani mumtendere.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 16