Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 16:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anafikanso ku Derbe ndi Lustra; ndipo taonani, panali wophunzira wina pamenepo, dzina lace Timoteo, amace ndiye Myuda wokhulupira; koma atate wace ndiye Mhelene.

2. Ameneyo anamcitira umboni wabwino abale a ku Lustra ndi Ikoniyo.

3. Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, cifukwa ca Ayuda amene anakhala m'maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wace anali Mhelene.

4. Pamene anapita kupyola pamidzi, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamulira atumwi ndi akuru a pa Yerusalemu.

5. Kotero Mipingoyo inalimbikitsidwa m'cikhulupiriro, nacuruka m'ciwerengo cao tsiku ndi tsiku.

6. Ndipo anapita pa dziko la Frugiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau m'Asiya; pamene anafika kundunji kwa Musiya,

7. anayesa kunka ku Bituniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleza;

8. ndipo pamene anapita pambali pa Musiya, anatsikira ku Trowa.

9. Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Makedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Makedoniya kuno, mudzatithangate ife.

10. Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kuturukirakunka ku Makedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 16