Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 15:8-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawacitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

9. ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'cikhulupiriro.

10. Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la akuphunzira gori, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

11. Koma tikhulupira tidzapulumuka mwa cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, monga iwo omwe.

12. Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Bamaba ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anacita nao pa amitundu.

13. Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati,Abale, mverani ine:

14. Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lace.

15. Ndipo mau a aneneri abvomereza pamenepo; monga kunalembedwa,

16. Zikatha izo ndidzabwera, Ndidzamanganso cihema ca Davine, cimene cinagwa;Ndidzamanganso zopasuka zace,Ndipo ndidzaciimikanso:

17. Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,Ndi amitundu onse amene dzina langa linachulidwa pa iwo,

18. Ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo ciyambire dzikolapansi.

19. Cifukwa cace ine ndiweruza, kuti tisabvute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,

20. koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

21. Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'midzi yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ace m'masunagoge masabata onse.

22. Pamenepo cinakomera atumwi ndi akuru ndi Eklesia yensekusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Bamaba; ndiwo Yuda wochedwa Barsaba, ndi Sila, akuru a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

23. Atumwi ndi abale akuru kwa abale a mwa amitundu a m'Antiokeya, ndi Suriya, ndi Kilikiya, tikulankhulani:

24. Popeza tamva kuti ena amene anaturuka mwa ife anakubvutani ndi mau, nasoceretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulira;

25. cinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Bamaba ndi Paulo,

26. anthu amene anapereka moyo wao cifukwa ca dzina la Yesu Kristu Ambuye wathu.

27. Tatumiza tsono Yuda ndi Sila, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 15