Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 15:3-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foinike ndi Samariya, nafotokozera cisanduliko ca amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.

4. Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akuru, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anacita nao.

5. Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge cilamulo ca Mose.

6. Ndipo anasonkhana atumwi ndi akuru kuti anene za mlanduwo.

7. Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupire.

8. Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawacitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

9. ndipo sanalekanitsa ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'cikhulupiriro.

10. Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi la akuphunzira gori, limene sanatha kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

11. Koma tikhulupira tidzapulumuka mwa cisomo ca Ambuye Yesu Kristu, monga iwo omwe.

12. Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Bamaba ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anacita nao pa amitundu.

13. Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati,Abale, mverani ine:

14. Sumeoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang'anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lace.

15. Ndipo mau a aneneri abvomereza pamenepo; monga kunalembedwa,

16. Zikatha izo ndidzabwera, Ndidzamanganso cihema ca Davine, cimene cinagwa;Ndidzamanganso zopasuka zace,Ndipo ndidzaciimikanso:

17. Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,Ndi amitundu onse amene dzina langa linachulidwa pa iwo,

18. Ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo ciyambire dzikolapansi.

19. Cifukwa cace ine ndiweruza, kuti tisabvute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,

20. koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 15