Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 15:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapandakudulidwa monga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.

2. Ndipo pamene Paulo ndi Bamaba anacitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Bamaba, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka ku Yerusalemu kwa atumwi ndi akuru kukanena za funsolo.

3. Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Foinike ndi Samariya, nafotokozera cisanduliko ca amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.

4. Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akuru, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anacita nao.

5. Koma anauka ena a mpatuko wa Afarisi okhulupira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge cilamulo ca Mose.

6. Ndipo anasonkhana atumwi ndi akuru kuti anene za mlanduwo.

7. Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m'kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupire.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 15