Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 14:14-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamene anamva atumwi Paulo ndi Bamaba, anang'amba zopfunda zao, natumphira m'khamu,

15. napfuula Dati, Anthuni, bwanji mucita zimenezi? ifenso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zacabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse ziri momwemo:

16. m'mibadwo, yakale iye adaleka mitundu yonse iyende m'njira mwao.

17. Koma sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anacita zabwino, nakupatsani inu zocokera kumwamba mvulaodi nyengoza zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi cakudya ndicikondwero.

18. Pakunena izo, anabvutika pakuletsa makamu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

19. Ndipo anafika kumeneko Ayuda kucokera ku Antiokeya ndi Ikoniyo; nakopa makamu, ndipo anamponya Paulomiyala, namguzira kunja kwa mudzi; namuyesa kuti wafa.

20. Koma pamene, anamzinga akuphunzirawo, anauka iye, nalowa m'mudzi; m'mawa mwace anaturuka ndi Bamaba kunka, ku Derbe.

21. Pamene analalikira Uthenga Wabwino pamudzipo, nayesa ambiri akuphunzira, anabwera ku Lustra ndi Ikoniyo ndi Antiokeya,

22. nalimbikitsa mitima ya akuphunzira, nadandauliraiwo kuti akhalebe m'cikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa m'ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.

23. Ndipo pamene anawaikira akuru mosankha mu Mpingo Mpingo, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, anaikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.

24. Ndipo anapitirira pa Pisidiya, nafika ku Pamfuliya.

25. Ndipo atalankhula mau m'Perge, anatsikira ku Ataliya;

26. komweko anacoka m'ngalawa kunka ku Antiokeya, kumene anaikizidwa ku cisomo ca Mulungu ku Ilchito imene adaimarizayo,

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 14