Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 14:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali pa Ikoniyo kuti analowa pamodzi m'sunagoge wa Ayuda, nalankhula kotero, kuti khamu lalikuru la Ayuda ndi Ahelene anakhulupira.

2. Koma Ayuda osamvefa anautsa mitima ya Ahelene kuti aipse abale athu.

3. Cifukwa cace anakhala nthawi yaikuru nanenetsa zolimba mtima mwa Ambuye, amene anacitira umboni mau a cisomo cace, napatsa zizindikiro ndi zozizwa kuti zicitidwe ndi manja ao.

4. Ndipo khamu la mudziwo linagawikana; ena analindi Ayuda, komaena anali ndi atumwi.

5. Ndipo pamene panakhala cigumukiro ca Ahelene ndi ca Ayuda ndi akuru ao, ca kuwacitira cipongwe ndi kuwaponya miyala,

6. iwo anamva, nathawira ku midzi ya Lukaoniya, Lustra ndi Derbe, ndi dziko lozungulirapo:

7. kumeneko ndiko Uthenga Wabwino.

8. Ndipo pa Lustra panakhala munthu wina wopanda mphamvu ya m'mapazi mwace, wopunduka cibadwire, amene sanayenda nthawi zonse.

9. Ameneyo anamva Paulo alinkulankhula; ndipo Paulo pomyang'anitsa, ndi kuona kuti anali ndi cikhulupiriro colandira naco moyo,

10. anati ndi mau akuru, Taimirira. Ndipo iyeyu anazunzuka, nayenda.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 14