Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 13:47-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

47. Pakuti kotero anatilamulira Ambuye ndi kuti,11 Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu,Kuti udzakhala iwe cipulumutso kufikira malekezero a dziko.

48. Ndipo pakumva ici amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupira onse amene anaikidwiratu ku moyo wosatha.

49. Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m'dziko lonse.

50. Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mudziwo, 12 nawautsira cizunzo Paulo ndi Bamaba, ndipo ana wapitikitsaiwom'malire ao.

51. Koma iwo, 13 m'mene adawasansirapfumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikoniyo,

52. Ndipo 14 akuphunzira anadzazidwa ndi cimwemwe ndi Mzimu Woyera.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 13