Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 13:20-34 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samueli mneneriyo.

21. Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa pfuko la Benjamini, zaka makumi anai.

22. Ndipo m'mene atamcotsa iye, anawautsira Davine akhale mfumu yao; amenenso anamcitira umboni, nati, Ndapeza Davine, mwana wa Jese, munthu wa pamtima panga, amene adzacita cifuniro canga conse.

23. Wocokera mu mbeu yace Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israyeli Mpulumutsi, Yesu;

24. Yohane atalalikiratu, asanafike iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israyeli.

25. Ndipo pakukwaniritsa njira yace Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ace.

26. Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a cipulumutso ici.

27. Pakuti iwo akukhala m'Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikira iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.

28. Ndipo ngakhale sanapeza cifukwa ca kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.

29. Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m'manda.

30. Koma Mulungu anamuukitsa iye kwa akufa;

31. ndipo 1 anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza iye pokwera ku Yerusalemu kucokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumcitira umboni tsopano kwa anthu.

32. Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa 2 lonjezano locitidwa kwa makolo;

33. kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa m'Salmo laciwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.

34. Ndipo kuti anamuukitsa iye kwa akufa, wosabweranso kueibvundi, anateropo, 3 Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davine.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 13