Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 13:1-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali aneneri ndi aphunzioo ku Antiokeya mu Mpingo wa komweko, ndiwo Barnaba, ndi Sumeoni, wonenedwa Nigeri, ndi Lukiya wa ku Kurene, Manayeni woleredwa pamodzi ndi Herode ciwangaco, ndi Saulo.

2. Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala cakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Bamaba ndi Saulo ku nchito imene odinawaitanirako.

3. Pamenepo, m'mene adasala cakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.

4. Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Selukeya; ndipo pocokerapo anapita m'ngalawa ku Kupro.

5. Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m'masunagoge a Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.

6. Ndipo m'mene anapitirira cisumbu conse kufikira Pafo, anapezapo munthu watsenga, mneneri wonyenga, ndiye Myuda, dzina lace Baryesu;

7. ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnaba ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

8. Koma Elima watsengayo (pakuti dzina lace litera posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupire.

9. Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,

10. nati, Wodzala ndi cinyengo conse ndi cenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa cilungamo conse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?

11. Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye liri pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapeoya dzuwa nthawi, Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamoka oaf una wina womgwira dzanja.

12. Pamenepo kazembe, pakuona cocitikacoanakhulupira, nadabwa naco ciphunzitso ca Ambuye.

13. Ndipo atamasula kucokera ku Pafo a ulendo wace wa Paulo anadza ku Perge wa ku Pamfuliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka ku Yerusalemu.

14. Koma iwowa, atapita pocokera ku Perge anafika ku Antiokeya wa m'Pisidiya; ndipo analowa m'sunagoge tsiku la Sabata, nakhala pansi.

15. Ndipo m'mene adatha kuwerenga cilamulo ndi aneneri akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 13