Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 12:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma nyengo imeneyo Herode mfumu anathira manja ena a m'Eklesia kuwacitira zoipa.

2. Ndipo adapha ndi lupanga Yakobo a mbale wa Yohane.

3. Ndipo pakuona kuti kudakondweretsa Ayuda, anaonjezapo nagwiranso Petro. Ndipo awo ndi masiku a mkate wopanda cotupitsa.

4. Ndipo m'mene adamgwira, anamuika m'ndende, nampereka kwa magulu anai a alonda, lonse anai anai, amdikire iye; ndipo anafuna kumturutsa kudza naye kwa anthu atapita Paskha.

5. Pamenepo ndipo Petro anasungika m'ndende; koma Eklesia anampempherera iye kwa Mulungu kosalekeza.

6. Ndipo pamene Herode anati amturutse, usiku womwewo Petro analikugona pakati pa asilikari awiri, womangidwa ndi maunyolo awiri; ndipo alonda akukhalapakhomoanadikira ndende.

7. Ndipo taonani, mngelo wa Ambuye anaimirirapo, ndipo kuunika kunawala mokhalamo iye; ndipo anakhoma Petro m'nthiti, namuutsa iye, nanena, Tauka msanga, Ndipo maunyolo anagwa kucoka m'manja mwace.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 12