1. Koma atumwi ndi abale akukhala m'Yudeya anamva kuti amitundunso adalandira mau a Mulungu.
2. Ndipo pamene Petro adakwera kudza ku Yerusalemu, iwo a kumdulidwe anatsutsana naye,
3. nanena kuti, Munalowa kwa anthu osadulidwa, ndi kudya nao.
4. Koma Petro anayamba kuwafotokozera cilongosolere, nanena,
5. Ndinali ine m'mudzi wa Yopa ndi kupemphera; ndipo m'kukomoka ndinaona masomphenya, cotengera cirikutsika, ngati cinsaru cacikuru cogwiridwa pa ngondya zace zinai; ndi kutsika kumwamba, ndipo cinadza pali ine;
6. cimeneco ndidacipenyetsetsa ndinacilingirira, ndipo ndinaona nyama za miyendo inai za padziko ndi zirombo, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga.
7. Ndipo ndinamvanso mau akunena ndi ine, Tauka Petro; ipha, nudye.
8. Koma ndinati, Iaitu, Ambuye; pakuti kanthu wamba, kapena konyansa sikanalowe m'kamwa mwanga ndi kale lonse.
9. Koma mau anayankha nthawi yaciwiri oturuka m'mwamba, Cimene Mulungu anaciyeretsa, usaciyesera cinthu wamba.
10. Ndipo ici cinacitika katatu; ndipo zinakwezekanso zonse kumwamba.