Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Macitidwe 10:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Koma Petro anati, Iaitu, Mbuye; pakuti sindinadya ine ndi kale lonse kanthu wamba ndi konyansa.

15. Ndipo mau anamdzeranso nthawi yaciwiri, Cimene Mulungu anayeretsa, usaciyesa cinthu wamba.

16. Ndipo cinacitika katatu ici; ndipo pomwepo cotengeraco cinatengedwa kunka kumwamba.

17. Ndipo pokayika-kayika Petro mwa yekha ndi kuti masomphenya adawaona akuti ciani, taonani, amuna aja otumidwa ndi Komeliyo, atafunsira nyumba ya Simoni, anaima pa cipata,

18. ndipo anaitana nafunsa ngati Simoni, wochedwanso Petro, acerezedwako.

19. Ndipo m'mene Petro analingirira za masomphenya, Mzimu ananena naye, Taona, amuna atatu akufuna iwe.

Werengani mutu wathunthu Macitidwe 10