Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:42-52 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo akadadza iye, ciwandaco cinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa, Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, naciritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wace.

43. Ndipo onse anadabwa pa ukulu wace wa Mulungu.Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazicita, iye anati kwa ophunzira ace,

44. Alowe mau ame: newa m'makutu anu; pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu.

45. Koma iwo sanadziwitse mau awa, ndipo anabisidwa kwa iwo, kuti asawadziwe; ndipo anaopa kumfunsa za mau awa.

46. Ndipo anayamba kutsutsana kuti wamkulu mwa iwo ndani.

47. Koma Yesu pakuona kutsutsana kwa mitima yao, anatenga kamwana, nakaimika pambali pace, nati kwa iwo,

48. Amene ali yense akalandire kamwana aka m'dzina langa alandira Ine; ndipo amene andilandira Ine alandira iye amene anandituma Ine; pakuti iye wakukhala wamng'onong'ono wa inu nonse, yemweyu ndiye wamkuru.

49. Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikuturutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, cifukwa satsatana nafe.

50. Koma Yesu anati kwa iye, Musamletse, pakuti iye amene satsutsana nanu athandizana nanu.

51. Ndipo panali, pamene anayamba kukwanira masiku akuti alandiridwe iye kumwamba, Yesu anatsimika kuloza nkhope yace kunka ku Yerusalemu,

52. natumiza amithenga patsogolo pace; ndipo ananka, nalowa m'mudzi wa Asamariya, kukamkonzera iye malo.

Werengani mutu wathunthu Luka 9