Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:39-44 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. ndipo onani, umamgwira iye mzimu, napfuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumcititsa thobvu pakamwa, nucoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye.

40. Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti auturutse; koma sanathe.

41. Ndipo Yesu anayankha, nati, Ha! obadwa inu osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji, ndi kulekerera inu? idza naye kuno mwana wako.

42. Ndipo akadadza iye, ciwandaco cinamgwetsa, ndi kumng'ambitsa, Koma Yesu anadzudzula mzimu wonyansawo, naciritsa mnyamata, nambwezera iye kwa atate wace.

43. Ndipo onse anadabwa pa ukulu wace wa Mulungu.Koma pamene onse analikuzizwa ndi zonse anazicita, iye anati kwa ophunzira ace,

44. Alowe mau ame: newa m'makutu anu; pakuti Mwana wa munthu adzaperekedwa m'manja a anthu.

Werengani mutu wathunthu Luka 9