Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:35-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

35. Ndipo munaturuka mau mumtambo nanena, Uyu ndiye Mwana wanga, wosankhidwayo; mverani iye.

36. Ndipo pakutero mauwo, Yesu anapezedwa ali yekha. Ndipo iwo anakhala cete, ndipo sanauza munthu ali yense masiku aja kanthu konse ka izo anaziona.

37. Ndipo panali, m'mawa mwace, atatsika m'phiri, khamu lalikuru la anthu linakomana naye.

38. Ndipo onani, anapfuula munthu wa m'khamulo, nanena, nati, Mphunzitsi, ndikupemphani, yang'anirani mwana wanga; cifukwa ndiye mmodzi yekha wa ine:

39. ndipo onani, umamgwira iye mzimu, napfuula modzidzimuka; ndipo umamng'amba iye ndi kumcititsa thobvu pakamwa, nucoka pa iye mwa unyenzi, numgola iye.

40. Ndipo ndinapempha ophunzira anu kuti auturutse; koma sanathe.

Werengani mutu wathunthu Luka 9