Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 9:26-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Pakuti amene ali yense: adzacita manyazi cifukwa ca Ine ndi mau anga, Mwana wa munthu adzacita manyazi cifukwa ca iye, pamene adzafika ndi ulemerero wace ndi wa Atate, ndi wa angelo oyera.

27. Koma Ine ndinena ndi inu zoonadi, Kuli ena a iwo akuimirira pano, amene sadzalawatu imfa, kufikira kuti adzaona Ufumu wa Mulungu.

28. Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.

29. Ndipo m'kupemphera kwace, maonekedwe a nkhope yace anasandulika, ndi cobvala cace cinayera ndi kunyezimira.

30. Ndipo onani, analikulankhulana nayeamuna awiri, ndiwo Mose ndi Eliya;

31. amene anaonekera m'ulemerero, nanenaza kumuka kwace kumene iye ati adzatsiriza ku Yerusalemu.

32. Koma Petro ndi iwo anali naye analemedwa ndi tulo; koma m'mene anayera m'maso ndithu, anaona ulemerero wace, ndi amuna awiriwo akuimirira ndi iye.

33. Ndipo panali polekana iwo aja ndi iye, Petro anati kwa Yesu, Ambuye, nkwabwino kuti tiri pano; ndipo timange misasa itatu, umodzi wa Inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya; wosadziwa iye cimene alikunena.

Werengani mutu wathunthu Luka 9