Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:15-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

16. Ndipo palibe munthu, atayatsa, nyali, aibvundikira ndi cotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pacoikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17. Pakuti palibe cinthu cobisika, cimene sicidzakhala coonekera; kapena cinsinsi cimene sicidzadziwika ndi kubvumbuluka.

18. Cifukwa cace yang'anirani mamvedwe anu; pakuti kudzapatsidwa kwa iye amene ali naco; ndipo kwa iye amene alibe cidzacotsedwa, cingakhale cija aoneka ngati ali naco.

19. Ndipo anadza kwa iye amace ndi abale ace, ndipo sanakhoza ku: mfika, cifukwa ca khamu la anthu.

20. Ndipo anamuuza iye, kuti, Amai wanu ndi abale anu alinkuima kunja, nafuna kuona Inu.

21. Koma iye anayankha, nati kwa iwo, Amai wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mau a Mulungu, nawacita.

22. Ndipo panali limodzi la masiku aja, iye analowa m'ngalawa, ndi ophunzira ace; nati kwa iwo, Tiolokere ku tsidya lija la nyanja; ndipo anakankhiramo.

23. Ndipo m'mene iwo anali kupita pamadzi, iye anagona tulo, Ndipo panyanja panatsikira namondwe wa mphepo; ndipo podzala ndi madzi, analimkuopsedwa.

Werengani mutu wathunthu Luka 8