Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 8:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ndipo zija zinagwa ku mingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi cuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.

15. Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.

16. Ndipo palibe munthu, atayatsa, nyali, aibvundikira ndi cotengera, kapena kuiika pansi pa kama; koma aiika pacoikapo, kuti iwo akulowamo aone kuunikaku.

17. Pakuti palibe cinthu cobisika, cimene sicidzakhala coonekera; kapena cinsinsi cimene sicidzadziwika ndi kubvumbuluka.

Werengani mutu wathunthu Luka 8