Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 7:41-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ace a marupiya mazana asanu, koma mnzace makumi asanu.

42. Popeza analibe cobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Cotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

43. Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa,

44. Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m'mene iye anaceukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m'nyumba yako, sunandipatsa madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lace.

45. Sunandipatsa mpsompsono wa cibwenzi; koma uyu sanaleka kupsompsonetsa mapazi anga, cilowere muno Ine.

46. Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma nyu anadzoza mapazi anga ndimafuta onunkhira bwmo.

47. Cifukwa cace, ndinena kwa iwe, Macimo ace, ndiwo ambiri, akhululukidwa; cifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang'ono, iye akonda pang'ono.

48. Ndipo anati kwa mkazi, Macimo ako akhululukidwa.

49. Ndipo iwo akuseama naye pacakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso macimo?

50. Ndipo Iyeanati kwa mkaziyo, Cikhulupiriro cako cakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

Werengani mutu wathunthu Luka 7