Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 7:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Pamene Yesu adamariza mau ace onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao.

2. Ndipo kapolo wa kenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.

3. Ndipo pamene iye ana-I mva za Yesu, anatuma kwa iye akuru a Ayuda, namfunsa iye kuti adze kupulumutsa kapolo wace.

4. Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumcitire ici;

5. pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ife sunagoge.

6. Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika iye tsono pafupi panyumba yace, kenturiyo anatuma kwa iye abwenzi ace, kunena naye, Ambuye, musadzibvute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa chindwi langa;

7. cifukwa cace ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzaciritsidwa.

8. Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera akuru anga, ndiri nao asilikari akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tacita ici, nacita.

9. Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeza, ngakhale mwa Israyeli, cikhulupiriro cacikuru cotere.

Werengani mutu wathunthu Luka 7