Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:33-38 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

33. Ndipo ngati muwacitira zabwino iwo amene akucitirani, inu zabwino, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti anthu ocimwa omwe amacita comweco.

34. Ndipo 2 ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti inde anthu ocimwa amakongoletsa kwa ocimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.

35. Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

36. Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

37. Ndipo 5 musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo mudzamasulidwa.

38. 6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

Werengani mutu wathunthu Luka 6