Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:29-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzace; ndi iye amene alanda copfunda cako, usamkanize malaya ako.

30. Munthu ali yense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

31. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

32. Ndipo 1 ngati muwakonda iwo akukondana ndinu, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti ocimwa omwe akonda iwo akukondana nao.

33. Ndipo ngati muwacitira zabwino iwo amene akucitirani, inu zabwino, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti anthu ocimwa omwe amacita comweco.

34. Ndipo 2 ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti inde anthu ocimwa amakongoletsa kwa ocimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.

35. Koma 3 takondanani nao adani anu, ndi kuwacitira zabwino, ndipo kongoletsani osayembekeza kanthu konse, ndipo mphotho yanu idzakhala yaikuru, ndipo 4 inu mudzakhala ana a Wamkurukuruyo; cifukwa iye acitira zokoma anthu osayamika ndi oipa.

36. Khalani inu acifundo monga Atate wanu ali wacifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.

37. Ndipo 5 musawatsutsa, ndipo simudzatsutsidwa. Masulani, ndipo mudzamasulidwa.

38. 6 Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti 7 kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

39. Ndipo iye ananenanso nao fanizo, 8 Kodi munthu wakhungu angathe kutsogolera mnzace wakhungu? kodi sadzagwa onse awiri m'mbuna?

40. 9 Wophunzira saposa mphunzitsi wace; koma yense, m'mene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wace.

Werengani mutu wathunthu Luka 6