Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:20-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

21. Odala inu akumva njala tsopano; cifukwa mudzakhuta. Odala inu akulira tsopano; cifukwa mudzaseka.

22. Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, cifukwa ca Mwana wa munthu.

23. Kondwerani tsiku lomweli, tumphani ndi cimwemwe; pakuti onani, mphotho zanu nzazikuru Kumwamba; pakuti makolo ao anawacitira aneneri zonga zomwezo.

24. Koma tsoka inu eni cuma! cifukwa mwalandira cisangalatso canu.

25. Tsoka inu okhuta tsopano! cifukwa mudzamva njala, Tsoka inu, akuseka tsopano! cifukwa mudzacita maliro ndi kulira misozi.

26. Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! pakuti makolo ao anawatero momwemo ananeri onama.

27. Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani zabwino iwo akuda inu,

28. dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akucitira inu cipongwe.

29. Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzace; ndi iye amene alanda copfunda cako, usamkanize malaya ako.

30. Munthu ali yense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.

31. Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.

Werengani mutu wathunthu Luka 6