Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 6:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Ndipo kutaca, anaitana ophunzira ace; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawachanso dzina lao atumwi:

14. Simoni, amene anamuchanso Petro, ndi Andreya mbale wace, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo,

15. ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wochedwa Zelote,

16. ndi Yuda mwana wa Yakobo, ndi Yudase Isikariote, amene anali wompereka iye.

17. Ndipo iye anatsika nao, naima pacidikha, ndi khamu lalikuru la ophunzira ace, nw unyinji waukuru wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anadza kudzamva iye ndi kudzaciritsidwa nthenda zao;

18. ndipo obvutidwa ndi mizimu yonyansa anaciritsidwa,

19. ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza iye; cifukwa munaturuka mphamvu mwa iye, niciritsa onsewa.

20. Ndipo iye anakweza maso ace kwa ophunzira ace, nanena, Odala osauka inu; cifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu Luka 6