35. Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.
36. Ndipo iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba cigamba ca maraya arsopano, naciphatika pa maraya akale; cifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi cigamba ca atsopanowo sicidzayenerana ndi akalewo.
37. Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; cifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.
38. Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m'matumba atsopano.
39. Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.