Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 5:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, iye analikuimirira m'mbali mwa nyanja ya Genesarete;

2. ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m'mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adaturuka m'menemo, nalikutsuka makoka ao.

3. Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.

4. Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.

5. Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa nchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.

6. Ndipo pamene anacita ici, anazinga unyinji waukuru wansomba; ndipo makoka ao analinkung'ambika;

7. ndipo anakodola anzao a m'ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.

8. Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mabondo ace a Yesu, nanena, Mucoke kwa ine, Ambuye, cifukwa ndine munthu wocimwa.

9. Pakuti cizizwo cidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;

10. ndipo cimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, amene anali anzace a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.

11. Ndipo m'mene iwo anakoceza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata iye.

Werengani mutu wathunthu Luka 5