Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 3:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo pa caka cakhumi ndi cisanu ca ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode ciwanga ca Galileya, ndi Filipo mbale wace ciwanga ca dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo ciwanga ca Abilene;

2. pa ukuru wansembe wao wa Anasi ndi Kayafa, panadza mau a Mulungu kwa Yohane mwana wa Zakariya m'cipululu.

3. Ndipo iye anadza ku dziko lonse la m'mbali mwa Yordano, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku cikhululukiro ca macimo;

4. monga mwalembedwa m'kalata wa mau a Yesaya mneneri, kuti,Mau a wopfuula m'cipululu,Konzani khwalala la Ambuye,Lungamitsani njira zace.

5. Cigwa ciri conse cidzadzazidwa,Ndipo phiri liri lonse ndi mtunda uti wonse zidzacepsedwa;Ndipo zokhota zidzakhala zolungama,Ndipo njira za zigoloondo zidzakhala zosalala;

6. Ndipo anthu onse adzaona cipulumutso ca Mulungu.

7. Cifukwa cace iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anaturukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?

8. Cifukwa cace balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.

9. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; cotero mtengo uli wonse wosabala cipatso cabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.

10. Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizicita ciani?

11. Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya acite comweco.

12. Ndipo amisonkho omwe anadza kudzabatizidwa, nati kwa iye, Mphunzitsi, ife tizicita ciani?

13. Koma iye anati kwa iwo, Musakapambe kanthu konse kakuposa cimene anakulamulirani.

Werengani mutu wathunthu Luka 3