Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:8-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Ndipo anakumbukila mau ace, nabwera kucokera kumanda,

9. nafotokozera zonse khumi ndi mmodziwo, ndi otsala onse omwe.

10. Koma panali Mariya wa Magadala, ndi Y ohana, ndi Mariya amace wa Yakobo, ndi akazi ena pamodzi nao amene ananena izi kwa atumwiwo.

11. Ndipo mau awa anaoneka pamaso pao ngati nkhani zacabe, ndipo sanamvera akaziwo.

12. Koma Petro ananyamuka nathamangira kumanda, ndipo powerama anaona nsaru zoyera pa zokha; ndipo anacoka nanka kwao, nazizwa ndi cija cidacitikaco.

13. Ndipo taonani, awiri a mwa iwo analikupita tsiku lomwelo kumudzi dzina lace Emau, wosiyana ndi Yerusalemu mastadiya makumi asanu ndi limodzi.

14. Ndipo iwowa anakambirana nkhani za izi zonse zidacitika.

15. Ndipo kunali m'kukambirana kwao ndi kufunsana, Yesu mwini anayandikira, natsagana nao.

16. Koma maso ao anagwidwa kuti asamzindikire iye.

17. Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zacisoni.

18. Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lace Kleopa, anayankha nati kwa iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m'Yerusalemu ndi wosazindikira zidacitikazi masiku omwe ano?

Werengani mutu wathunthu Luka 24