44. Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.
45. Ndipo 7 anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;
46. ndipo anati kwa iwo, 8 Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lacitatu;
47. ndi kuti kulalikidwe m'dzina lace kulapa ndi 9 kukhululukidwa kwa macimo kwa 10 mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.
48. 11 Inu ndinu mboni za izi.