Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:41-53 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Koma pokhala iwo cikhalire osakhulupirira cifukwa ca cimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, 3 Muli nako kanthu kakudya kuno?

42. Ndipo anampatsa iye cidutsu ca nsomba yokazinga.

43. Ndipo 4 anacitenga, nacidya pamaso pao.

44. Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

45. Ndipo 7 anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;

46. ndipo anati kwa iwo, 8 Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lacitatu;

47. ndi kuti kulalikidwe m'dzina lace kulapa ndi 9 kukhululukidwa kwa macimo kwa 10 mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu.

48. 11 Inu ndinu mboni za izi.

49. Ndipo onani, 12 Ine nditumiza pa inu lonjezano la Atate wanga; koma khalani inu m'mudzi muno, kufikira mwabvekedwa ndi mphamvu yocokera Kumwamba.

50. Ndipo anaturuka nao kufikira ku Betaniya; nakweza manja ace, nawadalitsa.

51. Ndipo kunali, 13 pakuwadalitsa iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.

52. Ndipo 14 anamlambira iye, nabwera ku Yerusalemu ndi cimwemwe cacikuru;

53. ndipo IS anakhala ci khalire m'Kacisi, nalikuyamika Mulungu, Amen.

Werengani mutu wathunthu Luka 24