Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:28-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

28. Ndipo anayandikira ku mudzi umene analikupitako; ndipo anacita ngati anafuna kupitirira.

29. Ndipo anamuumiriza iye, nati, Khalani ndi ife; pakuti kuli madzulo, ndipo dzuwa lapendekatu, Ndipo analowa kukhala nao.

30. Ndipo kunali m'mene iye anaseama nao pacakudya, anatenga mkate, naudalitsa naunyema, napatsa iwo.

31. Ndipo maso ao anatseguka, ndipo anamzindikira iye; ndipo anawakanganukira iye, nawacokera.

32. Ndipo anati wina kwa mnzace, Mtima wathu sunali wotentha m'kati mwathu nanga m'mene analankhula nafe m'njira, m'mene anatitseguliramalembo?

33. Ndipo ananyamuka nthawi yomweyo nabwera ku Yerusalemu, napeza khumi ndi mmodziwo, ndi iwo anali nao atasonkhana pamodzi,

34. nanena, Ambuye anauka ndithu, naonekera kwa Simoni.

35. Ndipo iwo anawafotokozera za m'njira, ndi umo anadziwika nao m'kunyema kwa mkate.

36. Ndipo pakulankhula izi iwowa, iye anaimirira pakati pao; nanena nao, Mtendere ukhale nanu.

37. Koma anaopsedwandi kucita mantha, 1 nayesa alikuona mzimu.

38. Ndipo anati kwa iwo, Mukhala bwanji obvutika? ndipo matsutsano am auka bwanji m'mtima mwanu?

39. Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine.

40. Ndipo m'mene ananena ici, anawaonetsera iwo manja ace ndi mapazi ace.

41. Koma pokhala iwo cikhalire osakhulupirira cifukwa ca cimwemwe, nalikuzizwa, anati kwa iwo, 3 Muli nako kanthu kakudya kuno?

42. Ndipo anampatsa iye cidutsu ca nsomba yokazinga.

43. Ndipo 4 anacitenga, nacidya pamaso pao.

44. Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.

45. Ndipo 7 anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo;

Werengani mutu wathunthu Luka 24