Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 24:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Ndipo mmodzi wa iwo, dzina lace Kleopa, anayankha nati kwa iye, Kodi iwe wekha ndiwe mlendo m'Yerusalemu ndi wosazindikira zidacitikazi masiku omwe ano?

19. Ndipo anati kwa iwo, Zinthu zanji? Ndipo anati kwa iye, lzi za Yesu Mnazarene, ndiye munthu mneneri wamphamvu m'nchito, ndi m'mau, pamaso pa Mulungu ndi anthu onse;

20. ndikuti ansembe akulu ndi akulu athu anampereka iye ku ciweruziro ca imfa, nampacika iye pamtanda.

21. Ndipo tinayembekeza ife kuti iye ndiye wakudzayo kudzaombola Israyeli, Komatunso, pamodzi ndi izi zonse lero ndilo tsiku lacitatu kuyambira zidacitika izi.

22. Komatu akazi enanso a mwa ife anatidabwitsa, ndiwo amene analawirira kumanda;

23. ndipo m'mene sanapeza mtembo wace, anadza, nanena kuti adaona m'masomphenya angelo, amene ananena kuti ali ndi moyo iye.

24. Ndipo ena a iwo anali nafe anacoka kunka kumanda, napeza monga momwe akazi adanena; koma Iyeyo sanamuona.

25. Ndipo iye anati kwa iwo, Opusa inu, ndiozengereza mtima kusakhulupirira zonse adazilankhula aneneri!

Werengani mutu wathunthu Luka 24