Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 23:42-50 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

42. Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukileni m'mene mulowa Ufumuwanu.

43. Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso.

44. Ndipo ora lace pamenepo linali ngati lacisanu ndi cimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lacisanu ndi cinai, ndipo dzuwa linada.

45. Ndipo nsaru yocinga ya m'Kacisi inang'ambika pakati.

46. Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace.

47. Ndipo 2 pamene kenturiyo anaona cinacitikaco, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.

48. Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ici, pamene anaona zinacitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pacifuwa.

49. Ndipo 3 omdziwa iye onse, ndi akazi amene adamtsata kucokera ku Galileya, anaima kutari, naona zinthu izi.

50. Ndipo taonani, munthu dzina lace Yosefe, ndiye mkuru wa mirandu, munthu wabwino ndi wolungama

Werengani mutu wathunthu Luka 23