Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Luka 20:19-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Ndipo alembi ndi ansembe akuru anafunafuna kumgwira ndi manja nthawi yomweyo; ndipo anaopa anthu; pakuti anazindikira kuti ananenera pa iwo fanizo ili.

20. Ndipo anamyang'anira, natumiza ozonda, amene anadzionetsera ngati olungama mtima, kuti akamkole pa mau ace, kotero kuti akampereke iye ku ukulu ndi ulamuliro wa kazembe.

21. Ndipo anamfunsa iye, nanena, Mphunzitisi, ife tidziwa kuti munena ndi kuphunzitsa kolunjika, ndi kusasamalira nkhope ya munthu, koma muphunzitsa njira ya Mulungu koonadi;

22. kodi kuloledwa kupereka msonkho kwa Kaisara, kapena iai?

23. Koma iye anazindikira cinyengo cao, nati kwa iwo,

24. Tandionetsani Ine rupiya latheka. Cithunzithunzi ndi colemba cace nca yani? Anati iwo, Ca Kaisara.

25. Ndipo iye anati kwa iwo, Cifukwa cace perekani kwa Kaisara zace za Kaisara, ndi kwa Mulungu zace za Mulungu.

26. Ndipo sanakhoza kugwira mauwo pamaso pa anthu; ndipo anazizwa ndi kuyankha kwace, nakhala cete.

27. Ndipo anadza kwa iye Asaduki ena, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; ndipo anamfunsa iye,

Werengani mutu wathunthu Luka 20